News that matters

Ogwira ntchito zothandizira pa sukulu ya Maryview for the Deaf ayamba kunyanyala ntchito kamba kamalipiro ochepa.

Posted by

CHRISTOPHER KADAMBO

Category

NEWS

Date

22 JAN 2025

img

K35,000 singakwane ufa.

Ogwira ntchito zothandizira pa sukulu ya Maryview for the deaf ayamba kunyanyala ntchito pofuna kuti malipiro awo akwezedwe. Mwa ogwira ntchitoyi pali osetsa ndikusamala pasukulupa komanso ophikira ana.

"Sitingakwanitse kumagwira ntchito kaamba koti malipiro tikulandira ndi ochepa. Tangoganizani K35,000 pamwezi. tikhala bwanji ndimmene zinthu zaduliramu." Adatero munthu m'modzi ogwira ntchito yemwe sanafune kuulura dzina lake. "Kulibwino tizikaitanira ma minibus kumsewuku." Adapitiliza mokhumudwa.

Okada.com idayetsa kuti iyankhulane ndi mphunzitsi wamkulu wasukuluyi Mr Kazembe koma adali mukachipinda komata kuyestsesa kuti zinthu ziyambirenso kuyenda bwino. Ophunzira mmodzi atafunsidwa kuti alongosole chomwe chavuta, iye amangogwira mmimba kumasonya kummawa zomwe mwina zimatanthauza kuti anawa sanadye kuyambira mmawa walero.

Kafukufuku wathu wasonyeza kuti anthuwa amalandira K35,000 pamwezi ngakhale boma linaika mulingo wa K50,000 ngati ndalama yochepetsesa yomwe munthu amayenera kulandira m'dziko muno. Maryview School for the Deaf ndi sukulu yomwe imaphunzitsa ana aulumali osamva m'boma la Chiradzulu. Sukuluyi ili ndi ana oposera zana limodzi.