Makina ovotera kapena kuwerengera kulibe.
Pamene dziko la Malawi likupita kuzitsankho pa 16 September 2025, Bungwe la MEC kudzera mwa mulangizi wawo m'boma la Chiradzulu lasutsa mphekesera zomwe zomwe zimamveka kuti anthu adzagwiritsa ntchito makina povota komanso powerengera mavoti.
"Ife a bungwe la MEC tikufuna tikutsimikizireni kuti tidzagwiritsa ntchito ma ballot paper omwe takhala tikugwiritsa ntchito kuyambira mu chaka cha 1993. Zoti kuli makina ovotera ndikuwerengesera mavoti anu ife sitikuzidziwa". Christopher Kadambo yemwe ndi m'modzi wa alangizi a MEC mu Chiradzulu adayankhula izi pa nkhwimbi la anthu lomwe linasonkhana pa Choda CCAP m'bomali zulo."
Mai Chipanda omwe adali pamalopa adali panopa ndiokhutira ndipo apita kukavota pa 16 September pano. Poonjezera apa Group Village Headman Sakwata adathokoza bungwe la MEC chifukwa chomva madandaulo awanthu ndipo adalonjezanso kuti uthengawu akhala akuubwereza kwa anthu awo mumisonkhano yakusogoloku.
M'boma la Chiradzulu anthu omwe adalembetsa kuti adzaponye voti ndi pafupifupi 147,000.